Marko 7:32-37 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

32. Ndipo anadza naye kwa Iye munthu wogontha, ndi wacibwibwi; ndipo anampempha Iye kuti aike dzanja pa iye.

33. Ndipo anampatula pa khamu la anthu pa yekha, nalonga zala zace m'makutu mwace, nalabvula malobvu, nakhudza lilime lace:

34. nagadamira kumwamba, nausa moyo, nanena naye, Elata, ndiko, Tatseguka.

35. Ndipo makutu ace anatseguka, ndi comangira lilime lace cinamasulidwa, ndipo analankhula cilunjikire.

36. Ndipo anawalamulira kuti asauze munthu, ali yense; koma monga momwe Iye anawalamulitsa momwenso makamaka analalikira kopambana.

37. Ndipo anadabwa kwakukurukuru, nanena, Wacita Iye zonse bwino; angakhale ogontha awamvetsa, ndi osalankhula awalankhulitsa.

Marko 7