Marko 4:22-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Pakuti kulibe kanthu kobisika, koma kuti kaonetsedwe; kapena kulibe kanthu kanakhala kam'tseri, koma kuti kakaululidwe.

23. Ngati munthu ali nao makutu akumva, amve.

24. Ndipo ananena nao, Yang'anirani cimene mukumva; ndi muyeso umene muyesera nao udzayesedwa kwa inu; ndipo kudzaonjezedwa kwa inu.

25. Pakuti kwa iye amene ali nako kanthu, kadzapatsidwa; ndipo kwa iye amene alibe kanthu, kadzacotsedwa ngakhale kanthu kali konse ali nako.

26. Ndipo ananena, Ufumu wa Mulungu uli wotero, monga ngati munthu akataya mbeu panthaka;

27. nakagona ndi kuuka, usiku ndi usana, ndipo mbeu zikamera, ndi kukula, iye sadziwa umo zicitira.

Marko 4