11. Ndipo Iye ananena nao, Kwa inu kwapatsidwa cinsinsi ca Ufumu wa Mulungu; koma kwa iwo ali kunja zonse zicitidwa m'mafanizo;
12. kuti kupenya apenye, koma asazindikire; ndipo kumva amve, koma asadziwitse; kuti pena angatembenuke, ndi kukhululukidwa.
13. Ndipo ananena nao, Simudziwa kodi fanizo ili? mukazindikira bwanji mafanizo onse?
14. Wofesa afesa mau.
15. Ndipo iwo ndiwo a m'mbali mwa njira mofesedwamo mau; ndipo pamene anamva, pomwepo akudza Satana nacotsa mau ofesedwa mwa iwo.
16. Ndipo momwemonso iwo ndiwo amene afesedwa pathanthwe, atamva mau, awalandira pomwepo ndi kusekera;
17. ndipo alibe mizu mwa iwo okha, koma akhala kanthawi; pamenepo pakudza masautso kapena mazunzo cifukwa ca mau, pomwepo akhumudwa.
18. Ndipo ena ndiwo akufesedwa kuminga; iwo ndiwo amene adamva mau,
19. ndipo malabadiro a dziko lapansi, ndi cinyengo ca cuma, ndi kulakalaka kwa zinthu zina, zilowamo, zitsamwitsa mau, ndipo akhala opanda cipatso.