5. Ndipo Yesu pakuona cikhulupiriro cao ananena ndi wodwala manjenje, Mwana, macimo ako akhululukidwa.
6. Koma anakhalapo ena a alembi akuganizira mumtima mwao,
7. Munthu amene atero bwanji? acita mwano; akhoza ndani kukhululukira macimo, koma mmodzi, ndiye Mulungu?
8. Ndipo pomwepo Yesu pozindikira mumtima mwace kuti alikuganizira comweco mwa iwo okha, ananena nao, Muganiza bwanji zinthu izi m'mitima yanu?