Marko 2:10-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Koma kuti mudziwe kuti Mwana wa munthu ali mwini ulamuliro wakukhululukira macimo pa dziko lapansi (ananena ndi wodwala manjenje),

11. Ndikuuza iwe, Nyamuka, senza mphasa yako, numuke kwanu.

12. Ndipo ananyamuka iye pomwepo, nasenza mphasa, naturuka pamaso pa iwo onse; kotero kuti anadabwa onse, nalemekeza Mulungu, nanena kuti, Zotere sitinaziona ndi kale lonse.

13. Ndipo anaturukanso kunka m'mbali mwa nyanja; ndipo linadza kwa Iye khamu lonse la anthu, ndipo anawaphunzitsa.

14. Ndipo pakumuka, anaona Levi mwana wa Alifeyu alikukhala polandira msonkho, ndipo ananena naye, Tsata Ine.

Marko 2