Marko 15:23-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. Ndipo anampatsa vinyo wosanganiza ndi mure; koma Iye sanamlandira.

24. Ndipo anampacika Iye, nagawana zobvala zace mwa iwo okha, ndi kucita maere pa izo, kuti adziwe yense adzatengaciani.

25. Ndipo panali ora lacitatu, ndipo anampacika Iye.

26. Ndipo lembo la mlandu wace linalembedwa pamwamba, MFUMU YAAYUDA.

27. Ndipo anapacika pamodzi ndi Iye acifwamba awiri; mmodzi ku dzanja lace lamanja ndi wina kulamanzere.[

28. ]

29. Ndipo iwo akupitirirapo anamcitira mwano, napukusa mitu yao, nanena, Ha! iwe wakupasula Kacisi, ndi kummanga masiku atatu,

30. udzipulumutse mwini, nutsike pamtanda.

31. Moteronso ansembe akuru anamtonza mwa iwo okha pamodzi ndi alembi, nanena, Anapulumutsa ena; sakhoza kudzipulumutsa yekha.

32. Atsike tsopano pamtanda, Kristu Mfumu ya Israyeli, kuti tione, ndi kukhulupirira. Ndipo iwo akupacikidwa naye anamlalatira.

33. Ndipo pofika ora lacisanu ndi cimodzi, panali mdima pa dziko lonse, kufikira ora lacisanu ndi cinai.

Marko 15