Marko 14:59-64 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

59. Ndipo ngakhale momwemo umboni wao sunalingana.

60. Ndipo mkulu wa ansembe ananyamuka pakati, namfunsa Yesu, nanena, Suyankha kanthu kodi? Nciani ici cimene awa alikucitira mboni?

61. Koma anakhala cete, osayankhakanthu. Mkulu wa ansembe anamfunsanso, nanena naye, Kodi Iwe ndiwe Kristu, Mwana wace wa Wolemekezeka?

62. Ndipo Yesu anati, Ndine amene; ndipo mudzaona Mwana wa munthu alikukhala ku dzanja lamanja la mphamvu, ndi kudza ndi mitambo ya kumwamba.

63. Ndipo mkulu wa ansembe anang'amba maraya ace, nanena, Tifuniranjinso mboni zina?

64. Mwamva mwano wace; muyesa bwanji? Ndipo onse anamtsutsa Iye kuti ayenera kufa.

Marko 14