Marko 13:32-37 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

32. Koma za tsiku ilo, kapena nthawi yace sadziwa munthu, angakhale angelo m'Mwamba, angakhale Mwana, koma Atate ndiye.

33. Yang'anirani, dikirani, pempherani: pakuti simudziwa nthawi yace.

34. Monga ngati munthu wa paulendo, adacoka kunyumba kwace, nawapatsa akapolo ace ulamuliro, kwa munthu ali yense nchito yace, nalamulira wapakhomo adikire.

35. Cifukwa cace dikirani; pakuti simudziwa inu nthawi yace yakubwera mwini nyumba, kapena madzulo, kapena pakati pausiku, kapena pakulira tambala, kapena mamawa;

36. kuti angabwere balamantha nakakupezani muli m'tulo.

37. Ndipo cimene ndinena ndi inu ndinena kwa onse, Dikirani.

Marko 13