1. Ha! golidi wagugadi; golidi woona woposa wasandulika;Miyala ya malo opatulika yakhutulidwa pa malekezero a makwalalaonse.
2. Ana a Ziyoni a mtengo wapatari, olingana ndi golidi woyengetsa,Angoyesedwa ngati mbiya zadothi zozipanga manja a woumba.
3. Angakhale ankhandwe amapatsa bere, nayamwitsa ana ao;Koma mwana wamkazi wa anthu amtundu wanga wasanduka wankhanza, ngati nthiwatiwa za m'cipululu.
4. Lilime la mwana woyamwa limamatira kumalakalaka kwace ndi ludzu;Ana ang'ono apempha mkate koma palibe wakuwanyemera.