Maliro 3:52-59 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

52. Ondida opanda cifukwa anandiinga ngati mbalame;

53. Anaononga moyo wanga m'dzenje, naponya mwala pamwambapaine;

54. Madzi anayenda pamwamba pa mutu panga, ndinati, dalikhidwa.

55. Ndinaitana dzina lanu, Yehova, ndiri m'dzenje lapansi;

56. Munamva mau anga; musabise khutu lanu popuma ndi popfuulaine.

57. Munayandikira tsiku la kukuitanani ine; munati, Usaope.

58. Ambuye munanenera moyo wanga mirandu yace; munaombola moyo wanga.

59. Yehova, mwaona coipa anandicitiraco, mundiweruzire;

Maliro 3