48. M'diso mwanga mutsikamitsinje ya madzi cifukwa ca mwana wamkazi wa anthu amtundu wanga woonongedwa,
49. Diso langa lingotsanulira osaleka, osapumula,
50. Kufikira Yehova adzazolika kumwamba ndi kuona;
51. Diso langa limvetsa moyo wanga zowawa cifukwa ca ana akazi onse a m'mudzi mwanga.
52. Ondida opanda cifukwa anandiinga ngati mbalame;
53. Anaononga moyo wanga m'dzenje, naponya mwala pamwambapaine;
54. Madzi anayenda pamwamba pa mutu panga, ndinati, dalikhidwa.
55. Ndinaitana dzina lanu, Yehova, ndiri m'dzenje lapansi;