3. Zoonadi amandibwezera-bwezera dzanja lace monditsutsa tsiku lonse.
4. Wagugitsa thupi langa ndi khungu langa, natyola mafupa anga.
5. Wandimangira zitando za nkhondo, wandizinga ndi ulembe ndi mabvuto.
6. Wandikhalitsa mumdima ngati akufakale.
7. Wanditsekereza ndi guta, sindingaturuke; walemeretsa unyolo wanga.
8. Inde, popfuula ine ndi kuitana andithandize amakaniza pemphero langa.
9. Watsekereza njira zanga ndi miya la yosema, nakhotetsa mayendedwe anga.
10. Andikhalira cirombo colalira kapena mkango mobisalira.
11. Wapambutsa njira zanga, nanding'amba; nandipululutsa.
12. Wathifula uta wace, nandiyesa polozetsa mubvi.
13. Walowetsa m'imso mwanga mibvi ya m'phodo mwace.
14. Ndasanduka wondiseka mtundu wanga wonse, ndi nyimbo yao tsiku lonse.
15. Wandidzaza ndi zowawa, wandikhutitsa civumulo.
16. Watyolanso mano anga ndi tinsangalabwi, wandikuta ndi phulusa.
17. Watarikitsanso moyo wanga ndi mtendere; ndinaiwala zabwino.
18. Ndipo ndinati, Mphamvu yanga yatha, osayembekezanso kanthu kwa Yehova.
19. Kumbukirani msauko Wanga ndi kusocera kwanga, ndizo civumulo ndi ndulu.
20. Moyo wanga uzikumbukirabe nuwerama mwa ine,
21. Ndiri naco ciyembekezo popeza ndilingalira ici ndiyembekeza kanthu.