11. Maso anga alefuka ndi misozi, m'kati mwanga mugwedezeka;Ciwindi canga cagwa pansi cifukwa ca kupasuka kwa mwana wamkazi wa anthu amtundu wanga;Cifukwa tiana ndi oyamwa akomoka m'makwalala a mudziwu.
12. Amati kwa amao, Tirigu ndi vinyo ali kuti?Pokomoka iwo ngati olasidwa m'makwalala a mudziwu,Potsanulidwa miyoyo yao pa zifuwa za amao.
13. Ndikucitire umboni wotani? ndikuyerekeze ndi ciani, mwana wamkazi wa Yerusalemu?Ndikulinganize ndi ciani kuti ndikutonthoze, namwaliwe, mwana wamkazi wa Ziyoni?Popeza akula ngati nyanja; ndani angakucize?
14. Aneneri ako anakuonera masomphenya acabe ndi opusa;Osaulula mphulupulu yako kuti abweze undende wako,Koma anakuonera manenero acabe ndi opambutsa.
15. Onse opita panjira akuombera manja:Atsonya, napukusira mitu yao pa mwana wamkazi wa Yerusalemu, nati,Kodi uwu ndi mudzi wochedwa wokongola, wangwiro, wokondweretsa dziko lonse?
16. Adani ako onse ayasamira pa iwe, Atsonya nakukuta mano, nati, Taumeza;Ndithu ili ndi tsiku tinaliyembekezalo, talipeza, taliona.
17. Yehova wacita comwe analingalira;Watsiriza mau ace, amene analamulira nthawi yakale;Wagwetsa osacitira cisoni;Wakondweretsa adani pa iwe,Wakweza nyanga ya amaliwongo ako.