1. Ambuye waphimbatu ndi mtambo mwana wamkazi wa Ziyoni, pomkwiyira!Wagwetsa pansi kucokera kumwamba kukoma kwace kwa Israyeli;Osakumbukira poponda mapazi ace tsiku la mkwiyo wace.
2. Yehova wameza nyumba zonse za Yakobo osazicitira cisoni;Wagumula malinga a mwana wamkazi wa Yuda mwa ukali wace;Wawagwetsera pansi, waipitsa ufumuwo ndi akalonga ace.