Maliro 1:5-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Amaliwongo ace asanduka akuru ace, adani ace napindula;Pakuti Yehova wamsautsa pocuruka zolakwa zace;Ana ace ang'ono alowa m'ndende pamaso pa adani ace.

6. Ulemu wace wonse wamcokera mwana wamkazi wa Ziyoni;Akalonga ace asanduka nswala zosapeza busa,Anayenda opanda mphamvu pamaso pa wompitikitsa.

7. M'masiku a msauko wace ndi kusocera kwaceYerusalemu ukumbukira zokondweretsa zace zonse zacikhalire;Pogwidwa anthu ace ndi mdaniyo popanda wakuupulumutsa,Adaniwo anamuona naseka mwacipongwe mabwinja ace.

8. Yerusalemu wacimwa kwambiri; cifukwa cace wasanduka cinthu conyansa;Onse akuulemekeza aupeputsa, pakuti auona wamarisece;Inde, uusa moyo, nubwerera m'mbuyo.

9. Udio wace unali m'nsaru zace; sunakumbukira citsiriziro cace;Cifukwa cace watsika mozizwitsa; ulibe wakuutonthoza;Taonani Yehova, msauko wanga, pakuti mdaniyo wadzikuzayekha.

10. Amaliwongo atambasulira manja ao pa zokondweretsa zace zonse;Pakuti waona amitundu atalowa m'malo ace opatulika,Amene munalamulira kuti asalowe mumsonkhano mwanu.

11. Anthu ace onse ausa moyo nafunafuna mkate;Ndi zokondweretsa zao agula zakudya kuti atsitsimutse moyo wao;Taonani, Yehova, nimupenye; pakuti ndasanduka wonyansa.

12. Kodi muyesa cimeneci cabe, nonsenu opita panjira?Penyani nimuone, kodi ciripo cisoni cina ngati cangaci amandimvetsa ine,Cimene Yehova wandisautsa naco tsiku la mkwiyo wace waukali?

Maliro 1