Macitidwe 8:8-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Ndipo panakhala cimwemwe cacikuru m'mudzimo.

9. Koma panali munthu dzina lace Simoni amene adacita matsenga m'mudzimo kale, nadabwitsa anthu a Samariya, ndi kunena kuti iye yekha ndiye munthu wamkuru;

10. ameneyo anamsamalira onsewo, kuyambira wamng'ono kufikira wamkuru, ndi kunena, Uyu ndiye mphamvu ya Mulungu, yonenedwa Yaikuru.

11. Ndipo anamsamalira iye, popeza nthawi yaikuru adawadabwitsa iwo ndi matsenga ace.

Macitidwe 8