4. Pamene unali nao, sunali wako kodi? ndipo pamene unaugulitsa sunali m'manja mwako kodi? bwanji cinalowa ici mumtima mwako? sunanyenga anthu, komatu Mulungu.
5. Koma Hananiya pakumva mau awa anagwa pansi namwalira: ndipo mantha akuru anagwera onse akumvawo.
6. Ndipo ananyamuka anyamata, namkulunga, namnyamula, naturuka naye, namuika.
7. Koma atapita monga maora atatu, ndipo mkazi wace, wosadziwa cidacitikaco, analowa.
8. Ndipo Petro ananena naye, Undiuze, ngati munagulitsa mundawo pa mtengo wakuti. Ndipo ananena, Inde, wakuti.
9. Koma Petro anati kwa iye, Munapangana pamodzi bwanji kuyesa Mzimu wa Ambuye? Taona, mapazi ao a iwo amene anaika mwamuna wako ali pakhomo, ndipo adzakunyamula kuturuka nawe.