Macitidwe 5:35-42 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

35. Ndipo anati kwa iwo, Amuna inu a Israyeli, kadzicenjerani nokha za anthu awa, cimene muti muwacitire.

36. Pakuti asanafike masiku ana anauka Teuda, nanena kuti ali kanthu iye mwini; amene anthu anaphatikana naye, ciwerengero cao ngati mazana anai; ndiye anaphedwa; ndi onse amene anamvera iye anamwazika, napita pacabe.

37. Atapita ameneyo, anauka Yuda wa ku Galileya, masiku a kulembedwa, nakopa anthu amtsate. Iyeyunso anaonongeka, ndi onse amene anamvera iye anabalalitsidwa.

38. Ndipo tsopano ndinena ndi inu, Lekani anthu amenewa, nimuwalole akhale; pakuti ngati uphungu umene kapena nchito iyi icokera kwa anthu, idzapasuka;

39. koma ngati icokera kwa Mulungu simungathe kuwapasula; kuti kapena mungapezeke otsutsana ndi Mulungu.

40. Ndipo anabvomerezana ndi iye; ndipo m'meheadaitana atumwi, anawakwapula nawalamulira asalankhule kuchula dzina la Yesu, ndipo anawamasula.

41. Pamenepo ndipo anapita kucokera ku bwalo la akuru, 1 nakondwera kuti anayesedwa oyenera kunyozedwa cifukwa ca dzinalo.

42. Ndipo masiku onse, m'Kacisi ndi m'nyumba, 2 sanaleka kuphunzitsa ndi kulalikira Kristu Yesu.

Macitidwe 5