5. andidziwa ine ciyambire, ngati afuna kucitapo umboni, kuti ndinakhala Mfarisi monga mwa mpatuko wolunjikitsitsa wa cipembedzero cathu.
6. Ndipo tsopano ndiimirira pano ndiweruzidwe pa ciyembekezo ca lonjezano limene Mulungu analicita kwa makolo athu;
7. kunkira komweko mafuko athu khumi ndi awiri, potumikira Mulungu kosapumula usiku ndi usana, ayembekeza kufikirako. Cifukwa ca ciyembekezo ici, Mfumu, andinenera Ayuda.
8. Muciyesa cinthu cosakhulupirika, cakuti Mulungu aukitsa akufa?
9. Inedi ndinayesa ndekha, kuti kundiyenera kucita zinthu zambiri zotsutsana nalo dzina la Yesu Mnazarayo.
10. Cimenenso ndinacita m'Yerusalemu: ndipo ndinatsekera ine oyera mtima ambiri m'ndende, popeza ndidalandira ulamuliro wa kwa ansembe akulu; ndiponso pophedwa iwo, ndinabvomerezapo.
11. Ndipo ndinawalanga kawiri kawiri m'masunagoge onse, ndi kuwakakamiza anene zamwano; ndipo pakupsa mtima kwakukuru pa iwo ndinawalondalonda ndi kuwatsata ngakhale kufikira ku midzi yakunja.