33. iwowo, m'mene anafika ku Kaisareya, anapereka kalata kwa kazembe, naperekanso Paulo kwa iye.
34. Ndipo m'mene adawerenga anafunsa acokera m'dziko liti; ndipo pozindikira kuti anali wa ku Kilikiya,
35. anati, Ndidzamva mlandu wako, pamene akukunenera afika. Ndipo analamulira kuti amdikire iye m'nyumba yamlandu ya Herode.