17. Ndipo kudzali m'masiku otsiriza, anena Mulungu,Ndidzathira ca Mzimu wansa pa thupi liri lonse,Ndipo ana anu amuna, ndi akazi adzanenera,Ndipo anyamata anu adzaona masomphenya,Ndi akulu anu adzalota maloto;
18. Ndiponso pa akapolo anga ndi pa adzakazi anga m'masiku awaNdidzathira ca Mzimu wanga; ndipo adzanenera.
19. Ndipo ndidzapatsa zodabwitsa m'thambo la kumwamba,Ndi zizindikilo pa dziko lapansi;Mwazi, ndi moto, ndi mpweya wautsi;
20. Dzuwa lidzasanduka mdima,Ndi mweziudzasanduka mwazi,Lisanadze tsiku la Ambuye,Lalikuru ndi loonekera;
21. Ndipo kudzali, kuti yense amene akaitana pa dzina laAmbuye adzapulumutsidwa.
22. Amuna inu Aisrayeli, mverani mau awa: Yesu Mnazarayo, mwamuna wocokera kwa Mulungu, wosonyezedwa kwa inu ndizimphamvu, ndi zozizwa, ndi zizindikilo, zimene Mulungu anazicita mwa iye pakati pa inu, monga mudziwa nokha;
23. ameneyo, woperekedwa ndi uphungu woikidwa ndi kudziwiratu kwa Mulungu, inu mwampacika ndi kumupha ndi manja a anthu osayeruzika;
24. yemweyo Mulungu anamuukitsa, atamasula zowawa za imfa, mwakuti sikunali kotheka kuti iye agwidwe nayo.
25. Pakuti Davine anena za Iye,Ndinaona Mbuye pamaso panga nthawi zonse;Cifukwa ali pa dzanja langa lamanja, kuti ndingasinthike;
26. Mwa ici unakondwera mtima wanga, ndipo linasangalala lilime langa;Ndipo thupi langanso lidzakhala m'ciyembekezo.