23. Pakuti popita, ndi kuona zinthu zimene muzipembedza, ndipezanso guwa la nsembe lolembedwa potere, KWA MULUNGU WOSADZIWIKA. Cimene mueipembedza osacidziwa, cimeneco ndicilalikira kwa inu.
24. Mulungu amene analenga dziko lapansi ndi zonse ziri momwemo, Iyeyo, ndiye mwini kumwamba ndi dziko lapansi, sakhala m'nyumba zakacisi zomangidwa ndi manja;
25. satumikidwa ndi manja a anthu, monga wosowa kanthu, popeza iye mwini apatsa zonse moyo ndi mpweya ndi zinthu zonse;