12. pocokera kumeneko tinafika ku Filipi, mudzi wa ku Makedoniya, waukuru wa m'dzikomo, wa miraga ya Roma; ndipojidagona momwemo masiku ena.
13. Tsiku la Sabata tinaturuka kumudzi kunka ku mbali ya mtsinje, kumene tinaganizira kuti amapempherako; ndipo tinakhala pansi ndi kulankhula ndi akazi amene adasonkhana,
14. Ndipo anatimva mkazi wina dzina lace Lidiya, wakugulitsa cibakuwa, wa ku mudzi wa Tiyatira, amene anapembedza Mulungu; mtima wace Ambuye anatsegula, kuti amvere zimene anazinena Paulo.
15. Pamene anabatizidwa iye ndi a pabanja pace anatidandaulira ife, kuti, Ngati mwandiyesera ine wokhulupirika kwa Ambuye, mulowe m'nyumba yanga, mugone m'menemo. Ndipo anatiumiriza ife.