Macitidwe 14:2-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Koma Ayuda osamvefa anautsa mitima ya Ahelene kuti aipse abale athu.

3. Cifukwa cace anakhala nthawi yaikuru nanenetsa zolimba mtima mwa Ambuye, amene anacitira umboni mau a cisomo cace, napatsa zizindikiro ndi zozizwa kuti zicitidwe ndi manja ao.

4. Ndipo khamu la mudziwo linagawikana; ena analindi Ayuda, komaena anali ndi atumwi.

5. Ndipo pamene panakhala cigumukiro ca Ahelene ndi ca Ayuda ndi akuru ao, ca kuwacitira cipongwe ndi kuwaponya miyala,

Macitidwe 14