1. Koma nyengo imeneyo Herode mfumu anathira manja ena a m'Eklesia kuwacitira zoipa.
2. Ndipo adapha ndi lupanga Yakobo a mbale wa Yohane.
3. Ndipo pakuona kuti kudakondweretsa Ayuda, anaonjezapo nagwiranso Petro. Ndipo awo ndi masiku a mkate wopanda cotupitsa.
4. Ndipo m'mene adamgwira, anamuika m'ndende, nampereka kwa magulu anai a alonda, lonse anai anai, amdikire iye; ndipo anafuna kumturutsa kudza naye kwa anthu atapita Paskha.