Macitidwe 10:9-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Koma m'mawa mwace, pokhala paulendo pao iwowa, m'mene anayandikira mudzi, Petro anakwera pachindwi kukapemphera, ngati pa ora lacisanu ndi cimodzi; ndipo anagwidwa njala, nafuna kudya;

10. koma m'mene analikumkonzera cakudya kudamgwera ngati kukomoka;

11. ndipo anaona pathambo padatseguka, ndi cotengera cirinkutsika, conga ngati cinsaru cacikuru, cogwiridwa pa ngondya zace zinai, ndi kutsikira padziko pansi;

12. m'menemo munali nyama za miyendo inai za mitundu yonse, ndi zokwawa za padziko ndi mbalame za m'mlengalenga.

13. Ndipo anamdzera mau, Tauka, Petro; ipha, nudye.

14. Koma Petro anati, Iaitu, Mbuye; pakuti sindinadya ine ndi kale lonse kanthu wamba ndi konyansa.

Macitidwe 10