Macitidwe 10:27-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

27. Ndipo pakukamba naye, analowa, napeza ambiri atasonkhana;

28. ndipo anati kwa iwo, Mudziwa inu nokha kuti sikuloledwa kwa munthu Myuda adziphatike kapena kudza kwa munthu wa mtundu wina; koma Mulungu anandionetsera ine ndisanenere ali yense ali munthu wamba kapena wonyansa;

29. cifukwa cacenso ndinadza wosakana, m'mene munatuma kundiitana. Pamenepo ndifunsa, mwandiitaniranji?

Macitidwe 10