25. Ndipo panali pakulowa Petro, Komeliyo anakomana naye, nagwa pa mapazi ace, namlambira.
26. Koma Petro anamuutsa iye, nanena, Nyamuka; inenso ndine munthu.
27. Ndipo pakukamba naye, analowa, napeza ambiri atasonkhana;
28. ndipo anati kwa iwo, Mudziwa inu nokha kuti sikuloledwa kwa munthu Myuda adziphatike kapena kudza kwa munthu wa mtundu wina; koma Mulungu anandionetsera ine ndisanenere ali yense ali munthu wamba kapena wonyansa;
29. cifukwa cacenso ndinadza wosakana, m'mene munatuma kundiitana. Pamenepo ndifunsa, mwandiitaniranji?