7. Koma anati kwa iwo, Sikuli kwa inu kudziwa nthawi kapena nyengo, zimene Atate anaziika m'ulamuliro wace wa iye yekha.
8. Komatu mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga m'Yerusalemu, ndi m'Yudeya lonse, ndi m'Samariya, ndi kufikira malekezero ace a dziko.
9. Ndipo m'mene adanena izi, ali cipenyerere iwo, ananyamulidwa; ndipo mtambo unamlandira iye kumcotsa kumaso kwao.
10. Ndipo pakukhala iwo cipenyerere kumwamba pomuka iye, taonani, amuna awiri obvala zoyera anaimirira pambali pao;
11. amenenso anati, Amuna a ku Galileya, muimiranji ndi kuyang'ana kumwamba? Yesu amene walandiridwa kunka Kumwamba kucokera kwa inu, adzadza momwemo monga munamuona alinkupita Kumwamba.