28. Ndipo pamene padatha ngati masiku asanu ndi atatu atanena mau amenewa, Iye anatenga Petro ndi Yohane ndi Yakobo apite naye, nakwera m'phiri kukapemphera.
29. Ndipo m'kupemphera kwace, maonekedwe a nkhope yace anasandulika, ndi cobvala cace cinayera ndi kunyezimira.
30. Ndipo onani, analikulankhulana nayeamuna awiri, ndiwo Mose ndi Eliya;
31. amene anaonekera m'ulemerero, nanenaza kumuka kwace kumene iye ati adzatsiriza ku Yerusalemu.