Luka 4:35-38 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

35. Ndipo Yesu anamdzudzula iye, nanena, Tonthola, nuturuke mwa iye. Ndipo ciwandaco m'mene cinamgwetsa iye pakati, cinaturuka mwa iye cosampweteka konse.

36. Ndipo anthu onse anadabwa, nalankhulana wina ndi mnzace, nanena, Mau amenewa ali otani? cifukwa ndi ulamuliro ndi mphamvu angolamulira mizimu yonyansa, ndipo ingoturuka.

37. Ndipo mbiri yace ya iye inafalikira ku malo onse a dziko Ioyandikira.

38. Ndipo iye ananyamuka kucokera m'sunagoge, nalowa m'nyumba ya Simoni. Koma momwemo munali mpongozi wace wa Simoni, anagwidwa ndi nthenda yolimba yamalungo; ndipo anampempha Yesu za iye.

Luka 4