Luka 22:43-47 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

43. Ndipo anamuonekera iye 1 mngelo wa Kumwamba namlimbitsa iye.

44. Ndipo 2 pokhala iye m'cipsinjo mtima anapemphera kolimba koposa ndithu: ndi thukuta lace linakhala ngati madontho akuru a mwazi alinkugwa pansi.

45. Ndipo pamene ananyamuka pakupemphera anadza kwa ophunzira, nawapeza ali m'tulo ndi cisoni,

46. ndipo anati kwa iwo, Mugoneranji? Ukani, 3 pempherani kuti mungalowe m'kuyesedwa.

47. Pamene iye anali cilankhulire, taonani, khamu la anthu, ndipo iye wochedwa Yudase, mmodzi wa khumi ndi awiriwo, anawatsogolera; nayandikira Yesu kumpsompsona iye.

Luka 22