Luka 21:3-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Ndipo iye anati, Zoonadi ndinena kwa inu, wamasiye uyu waumphawi anaikamo koposa onse;

4. pakuti onse amenewa anaika mwa unyinji wao pa zoperekazo; koma iye mwa kusowa kwace anaikamo za moyo wace, zonse anali nazo.

5. Ndipo pamene ena analikunena za Kacisiyo, kuti anakonzeka ndi miyala yokoma ndi zopereka, anati iye,

6. Zinthu izi muziona, adzafika masiku, pamenepo sudzasiyidwa pano mwala pa mwala unzace, umene sudzagwetsedwa.

Luka 21