34. Ndipo Simeoni anawadalitsa, nati kwa Mariya amace, Taona, Uyu waikidwa akhale kugwa ndi kunyamuka kwa anthu ambiri mwa. Israyeli; ndipo akhale cizindikilo cakutsutsana naco;
35. eya, ndipo lupanga lidzakupyoza iwe moyo wako; kuti maganizo a m'mitima yambiri akaululidwe.
36. Ndipo panali Anna, mneneri wamkazi, mwana wa Fanueli, wa pfuko la Aseri; amene anali wokalamba ndithu, nakhala ndi mwamuna wace, kuyambira pa unamwali wace,
37. zaka zisanu ndi ziwiri, ndipo anali wamasiye wa kufikira zaka zace: makumi asanu ndi atatu mphambu zinai, amene sanacoka kuKacisi, wotumikira Mulungu ndi kusala kudya ndi kupemphera usiku ndi usana.