Luka 16:1-2 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo iye ananenanso kwa ophunzira ace, Panali munthu mwini cuma, anali ndi kapitao wace; ndipo ameneyu ananenezedwa kwa iye kuti alikumwaza cuma cace.

2. Ndipo anamuitana, nati kwa iye, ici ndi ciani ndikumva za iwe? Undiwerengere za ukapitao wako; pakuti sungathe kukhalabe kapitao.

Luka 16