Luka 14:13-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Koma pamene ukonza phwando uitane aumphawi, opunduka, otsimphina, akhungu;

14. ndipo udzakhala wodala; cifukwa iwo alibe cakubwezera iwe mphotho; pakuti idzabwezedwa mphotho pa kuuka kwa oiungama.

15. Ndipo pamene wina wa iwo akuseama pacakudya pamodzi ndi iye anamva izi, anati kwa iye, Wodala iye amene adzadya mkate mu Ufumu wa Mulungu.

16. Koma anati kwa iye, Munthu wina anakonza phwando lalikuru; naitana anthu ambiri;

Luka 14