30. Ndipo onani, alipo akuthungo amene adzakhala oyamba, ndipo alipo oyamba adzakhala akuthungo.
31. Nthawi yomweyo anadzapo Afarisi ena, nanena kwa iye, Turukani, cokani kuno; cifukwa Herode afuna kupha lou.
32. Ndipo iye anati kwa iwo, Pitani kauzeni nkhandweyo, Taonani, nditurutsa ziwanda, nditsiriza maciritso lero ndi mawa, ndipo mkuca nditsirizidwa.