Luka 11:45-48 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

45. Ndipo mmodzi wa acilamulo anayankha, nanena kwa iye, Mphunzitsi, ndi kunena izi, mutitonza ifenso.

46. Ndipo anati, Tsoka inunso, acilamulo inul cifukwa musenzetsa anthu akatundu osautsa ponyamula, ndipo inu nomwe simukhudza akatunduwo ndi cala canu cimodzi.

47. Tsoka inu! cifukwamumanga za pa manda a aneneri, ndipo makolo anu anawapha.

48. Comweco muli mboni, ndipo mubvomera nchito za makolo anu; cifukwa iwotu anawapha, koma inu muwamangira iwo zapamanda.

Luka 11