Levitiko 9:18-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Anaphanso ng'ombe, ndi nkhosa yamphongoyo, ndizo nsembe zoyamika za anthu; ndi ana a Aroni anapereka kwa iye mwaziwo, ndipo anauwaza pa guwa la nsembe pozungulira, ndi mafuta a ng'ombe;

19. ndi a nkhosa, ndi mcira wamafuta, ndi cophimba matumbo, ndi imso, ndi cokuta ca mphafa;

20. ndipo anaika mafuta pa ngangazo, natentha mafutawo pa guwa la nsembe.

21. Ndipo Aroni anaweyula ngangazo ndi mwendo wathako wa ku dzanja lamanja zikhale nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; monga iye anauza Mose.

22. Ndipo Aroni anakweza dzanja lace kulozera anthu, nawadalitsa; natsika kuja anapereka nsembe yaucimo, ndi nsembe yopsereza, ndi nsembe zoyamika.

23. Ndipo Mose ndi Aroni analowa ku cihema cokomanako, naturuka, nadalitsa anthu; ndipo ulemero wa Yehova unaonekera kwa anthu onse.

24. Ndipo unaturuka mota pamaso ya Yehova, nunyeketsa nsembe yopsereza ndi mafuta pa guwa la nsembe; ndipo pakuciona anthu onse anapfuula, nagwa nkhope zao pansi.

Levitiko 9