Levitiko 4:27-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

27. Ndipo akacimwa wina wa anthu a m'dziko, osati dala, pa cina ca zinthu ziri zonse aziletsa Yehova, naparamula;

28. akamdziwitsa kucimwa kwace adacimwako, azidza naco copereka cace mbuzi yaikazi, yopanda cirema, cifukwa ca kucimwa kwace adakucita.

29. Aike dzanja lace pamutu pa nsembe yaucimo, naiphe nsembe yaucimo pamalo pa nsembe yopsereza.

30. Ndipo wansembe atengeko mwazi ndi cala cace, nauike pa nyanga za guwa la nsembe yopsereza, ndi kuthira mwazi wace wonse patsinde pa guwa la nsembe.

31. Nacotse mafuta ace onse, monga umo amacotsera mafuta pa nsembe yoyamika; ndipo wansembeyo awatenthe pa guwa la nsembe akhale pfungo lokoma la kwa Yehova; ndi wansembe amcitire comtetezera, ndipo adzakhululukidwa.

32. Ndipo akadza nayo nkhosa, ndiyo copereka cace, ikhale nsembe yaucimo, azidza nayo yaikazi, yopanda cirema.

33. Naike dzanja lace pa mutu wa nsembe yaucimo, ndi kuipha ikhale nsembe yaucimo pamalo pophera nsembe yopsereza.

Levitiko 4