22. Ndipo pakukolola dzinthu za m'dziko mwanu, usamakololetsa m'mphepete mwa munda wako, nusamakunkha khunkha; uzisiyire wosauka ndi mlendo; Ine ndine Yehova Mulungu wako.
23. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,
24. Nena ndi ana a Israyeli, ndi kuti, Mwezi wacisanu ndi ciwiri, tsiku loyamba la mweziwo, muzipumula, ndiko cikumbutso ca kuliza malipenga, msonkhano wopatulika.
25. Musamagwira nchito ya masiku ena; mubwere nayo nsembe yamoto ya Yehova.
26. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,
27. Komatu, tsiku lakhumi la mwezi uwu wacisanu ndi ciwiri, ndilo tsiku la citetezero; mukhale nao msonkhano wopatulika, ndipo mudzicepetse; ndi kubwera nayo nsembe yamoto kwa Yehova.