14. Musamadya mkate, kapena tirigu wokazinga, kapena ngala zaziwisi, kufikira tsiku lomweli, kufikira mutadza naco copereka ca Mulungu wanu; ndilo lemba losatha mwa mibadwo yanu m'nyumba zanu zonse.
15. Ndipo mudziwerengere kuyambira tsiku lotsata Sabata, kuyambira tsikuli mudadza nao mtolo wa nsembe yoweyula; pakhale masabata asanu ndi awiri amphumphu;
16. muwerenge masiku makumi asanu kufikira tsiku lotsata sabata lacisanu ndi ciwiri; pamenepo mubwere nayo kwa Yehova nsembe ya ufa watsopano.
17. Muturuke nayo m'zinyumba zanu mikate iwiri ya nsembe yoweyula, ikhale ya awiri a magawo khumi a efa; ikhale ya ufa wosalala, yopanga ndi cotupitsa, zipatso zoyamba za Yehova.
18. Ndipo mubwere nao pamodzi ndi mikate, ana a nkhosa asanu ndi awiri, opanda cirema a caka cimodzi, ndi ng'ombe yamphongo imodzi, ndi nkhosa zamphongo ziwiri; zikhale nsembe yopsereza ya Yehova, pamodzi ndi nsembe yao yaufa, ndi nsembe zao zothira, ndizo nsembe yamoto ya pfungo lokoma la Yehova.