7. Ndipo copereka cako cikakhala nsembe yaufa ya mumphika, cikhale ca ufa wosalala ndi mafuta.
8. Ndipo ubwere nayo nsembe yaufa yopangika ndi izi kwa Yehova; ndipo atabwera naco kwa wansembe, iyeyo apite naco ku guwa la nsembe.
9. Ndipo wansembeyo atengeko cikumbutso pa nsembe yaufa, nacitenthe pa guwa la nsembe; ndico nsembe yamoto ya pfungo lokoma la kwa Yehova.
10. Ndipo cotsalira ca nsembe yaufa cikhale ca Aroni ndi ana ace; ndico copatulikitsa ca nsembe zamoto za Yehova.
11. Nsembe iri yonse yaufa, imene mubwera nayo kwa Yehova, isapangike ndi cotupitsa, pakuti musamatenthera Yehova nsembe yamoto yacotupitsa, kapena yauci.