7. Ndipo asamapheranso ziwanda nsembe zao, zimene azitsata ndi cigololo. Ili liwakhalire lemba losatha mwa mibadwo yao.
8. Ndipo uzinena nao, Munthu ali yense wa mbumba ya Israyeli, kapena mlendo wakugonera pakati panu, amene apereka nsembe yopsereza kapena nsembe yophera,
9. osadza nayo ku khomo la cihema cokomanako, kuiphera Yehova; amsadze munthuyu kumcotsa kwa anthu a mtundu wace.
10. Ndipo munthu ali yense wa mbumba ya Israyeli, kapena mlendo wogonera pakati panu, wakudya mwazi uli wonse; nkhope yanga idzatsutsana naye munthu wakudya mwaziyo, ndi kumsadza kumcotsa kwa anthu a mtundu wace.