Levitiko 15:3-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Ndipo kudetsedwa kwa kukha kwace ndiko: ngakhale cakukhaco cituruka m'thupi mwace, ngakhale caleka m'thupi mwace, ndiko kumdetsa kwace.

4. Kama ali yense agonapo wakukhayo ali wodetsedwa; ndi cinthu ciri conse acikhalira ciri codetsedwa.

5. Ndipo munthu ali yense wakukhudza kama wace azitsuka zobvala zace, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo,

6. Ndipo iye wakukhalira cinthu ciri conse adacikhalira wakukhayo atsuke zobvala zace, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

7. Ndipo iye wakukhudza thupi la uyo wakukhayo atsuke zobvala zace, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

8. Ndipo wakukhayo akalabvulira wina woyera; pamenepo atsuke zobvala zace, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

9. Ndipo mbereko iri yonse akwerapo wakukhayo iri yodetsedwa.

10. Ndipo munthu ali yense akakhudza kanthu kali konse kadali pansi pace adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; ndipo iye wakunyamula zimenezo atsuke zobvala zace, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

11. Ndipo munthu ali yense wakukhayo akamkhudza, osasambatu m'manja m'madzi, atsuke zobvala zace, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

Levitiko 15