14. Ndipo wansembe atengeko mwazi wa nsembe yoparamula, ndipo wansembe aupake pa ndewerere ya khutu la ku dzanja lamanja la iye wakuti ayeretsedwe, ndi pa cala cacikuru ca dzanja lace lamanja, ndi pa cala cacikuru ca phazi lace la ku dzanja lamanja;
15. ndipo wansembe atengeko muyeso wa mafuta, nawathire pa cikhato ca dzanja lace lamanzere la iye mwini;
16. ndipo wansembe abviike cala cace ca dzanja lace lamanja ca iye mwini m'mafuta ali m'dzanja lace lamanzere, nawaze mafuta kasanu ndi kawiri ndi cala cace pamaso pa Yehova;
17. ndipo wansembe apakeko mafuta okh a ria m'dzanja lace pa ndewerere ya khutu la ku dzanja lamanja la iye wakuti ayeretsedwe, ndi pa cala cacikuru ca dzanja lace lamanja, ndi pa cala cacikuru ca phazi lace la ku dzanja lamanja, pa mwazi wa nsembe yoparamula;