4. Koma ngati cikanga cikhala cotuwa pa khungu la thupi lace, ndipo cikaoneka cosapitirira khungu, ndi tsitsi lace losasanduka loyera, pamenepo wansembe ambindikiritse wanthendayo masiku asanu ndi awiri;
5. ndipo wansembe amuonenso tsiku lacisanu ndi ciwiri; ndipo taonani, monga momwe apenyera iye, nthenda yaima, nthenda siinapitirira pakhungu, pamenepo wansembe ambindikiritsenso masiku asanu ndi awiri ena;
6. ndipo wansembe amuonenso tsikulacisanu ndi ciwiri, ndipo taonani, nthenda yazimba yosapitirira khungu nthendayi, pamenepo wansembe amuche iye woyera, ndiyo nkhanambo cabe; ndipo atsuke zobvala zace, ndiye woyera;
7. koma nkhanambo ikapitirira khungu, atadzionetsakwa wansembe kuti achedwe woyera, adzionetsenso kwa wansembe;
8. ndipo wansembe aone, ndipo taonani, ngati nkhanambo yapitirira khungu, wansembe amuche wodetsedwa, ndilo khate.