Levitiko 10:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo ana a Aroni, Nadabu ndi Abihu anatenga yense mbale yace ya zofukiza, naikamo moto, naikapo cofukiza, nabwera nao pamaso pa Yehova moto wacilendo, umene sanawauza.

2. Ndipo panaturuka moto pamaso pa Yehova, nuwatha, nafa iwo pamaso pa Yehova.

3. Ndipo Mose anati kwa Aroni, Ici ndi cimene Yehova ananena, ndi kuti, Mwa iwo akundiyandikiza ndipatulidwa Ine, ndi pamaso pa anthu onse ndilemekezedwa. Ndipo Aroni anakhala cete.

4. Ndipo Mose anaitana Misayeli ndi Elizafana, ana a Uziyeli, mbale wa atate wa Aroni, nanena nao, Senderani pafupi, nyamulani abale anu muwacotse pakhomo pa malo opatulika kumka nao kunja kwa cigono.

5. Pamenepo anasendera pafupi, nawanyamula osawabvula maraya ao a m'kati, kumka nao kunja kwa cigono, monga Mose adauza.

Levitiko 10