15. Ndipo wansembe abwere naco ku guwa la nsembe, namwetule mutu wace, naitenthe pa guwa la nsembe; ndi mwazi wace aukamulire pa mbali ya guwa la nsembe,
16. nacotse citsokomero, ndi cipwidza cace, nazitaye kufupi kwa guwa la nsembe, kum'mawa, kudzala;
17. nang'ambe mapiko ace osawacotsa konse ai; ndipo wansembeyo aitenthe pa guwa la nsembe, pa nkhuni ziri pamoto; ndiyo nsembe yopsereza, nsembe yamoto, ya pfungo lokoma la kwa Yehova.