Hoseya 6:6-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Pakuti ndikondwera naco cifundo, si nsembe ai; ndi kumdziwa Mulungu koposa nsembe zopsereza.

7. Koma iwo analakwira cipangano ngati Adamu, m'mene anandicitira monyenga.

8. Gileadi ndiwo mudzi wa ocita zoipa, wa mapazi a mwazi.

9. Ndipo monga magulu a mbala alalira munthu, momwemo msonkhano wa ansembe amapha pa njira ya ku Sekemu; indedi acita coipitsitsa.

10. M'nyumba ya Israyeli ndinaona cinthu coopsetsa; pamenepo pali citole ca Efraimu; Israyeli wadetsedwa.

11. Akuikidwiratunso nyengo yakukolola, Yuda iwe, pamene ndikabwezanso undende wa anthu anga.

Hoseya 6